M'miyoyo yathu yakuthupi komanso yauzimu, nthawi zonse pamakhala mayesero ndi zopinga zambiri. Kale, pamene Aisraele anakumana ndi mayesero aakulu—chipululu chopanda madzi ndi chakudya ndi dziko la Kanani lomwe linali ndi zimphona, Yoswa ndi Kalebe anaika chiyembekezo chawo mwa Mulungu yekha. Mofanana ndi iwo, ifenso tifunika chikhulupiriro kuti tiwone khomo la chiyembekezo lomwe Mulungu watitsegulira pakati pa mavuto.
Monga momwe Yesu anaukitsidwira ndi kukwera kumwamba, Mulungu anatsegula khomo la chiyembekezo ku ufumu wakumwamba kwa oyera mtima a Mpingo oyamba omwe anataya mtima pamene Yesu anapachikidwa, ndipo monga momwe Yesu anasonyezera Petro, yemwe sanagwire kanthu usiku wonse, chozizwitsa chomwe chimachitika tikamachita zomwe Iye wanena, leronso, mawu a Khristu Ahnsahnghong, akuti, “Uthenga Wabwino udzalalikidwa padziko lonse lapansi,” adzakwaniritsidwa ndithu.
Yehova, mundidziwitse chimaliziro changa, ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati; ndidziwe malekezero anga. Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira chiyani? Chiyembekezo changa chili pa Inu. Masalimo 39:4–7
Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka. Ndipo Uthenga uwu Wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro. Mateyu 24:13–14
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi