Yoswa ndi Kalebe anali ndi chikhulupiriro cholimba m’malonjezo a Mulungu.
Ngakhale kuti ku Kanani kunali zimphona kumene Mulungu analonjeza, Yoswa ndi Kalebe anakhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu adzawapatsadi dzikolo.
Mofanana ndi Kalebe amene sanazengereze kupita kukagonjetsa dziko lolonjezedwa ngakhale ali ndi zaka 85, m’nthawi ino, tiyeneranso kuyembekezera kumwamba ndi chikhulupiriro chofanana ndi cha Yoswa ndi Kalebe.
Monga Mulungu anali ndi Yoswa ndi Kalebe paulendo wawo wonse wopita ku Kanani, lero, tikhoza kumva kuti Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi nthawi zonse amatsegula njira kuti uthenga wabwino wa Mpingo wa Mulungu ufalikire mofulumira padziko lonse lapansi.
“Simudzalowa inu m’dzikolo, ndinakwezapo
dzanja langa kukukhalitsani m’mwemo,
koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi
Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.”
Numeri 14: 30
Ndipo atafa Mose mtumiki wa Yehova,
Yehova anati kwa Yoswa mwana wa
Nuni mnyamata wa Mose,
“. . . Khala wamphamvu, nulimbike mtima,
pakuti udzagawira anthu awa dzikoli
likhale cholowa chao, ndilo limene
ndinalumbirira makolo ao kuwapatsa. . . .
pakuti Yehova Mulungu wako
ali ndi iwe kulikonse umukako.”
Yoswa 1:1–9
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi