Abrahamu anapereka chachikhumi kwa Melekizedeki amene anam’dalitsa kudzera mu mkate ndi vinyo, ndipo Davide analosera kuti “wansembe wamuyaya wotsatira dongosolo la Melkizedeki ndi Mulungu.” Komanso, mtumwi Paulo anachitira umboni za Khristu amene adzabweranso m’Nthawi ya Mzimu Woyera pachipulumutso cha anthu, pofotokoza kuti “Melkizedeki alibe atate kapena amayi ake , kapena mawerengedwe achibadwidwe.
Melkizedeki wa Chipangano Chakale anapatsa Abrahamu mdalitso wakuthupi kudzera mu mkate ndi vinyo. Momwemonso, Yesu anapereka mdalitso wa chikhululukiro cha machimo ndi moyo wosatha kudzera mu mkate ndi vinyo wa Paskha wa Pangano Latsopano. Khristu Ahnsahnghong anachitira umboni kuti Iye ndi Mulungu amene anabwera mu dongosolo la Melkizedeki, pobwezeretsa Paskha wa Pangano Latsopano yemwe anathetsedwa kwa zaka 1,600.
Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu kukomana naye, atabwera anatha kuwakantha Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye,…Ndipo Melkizedeki mfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo… Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.
Genesis 14:17–20
Ndipo ophunzira anachita monga Yesu anawauza, nakonza Paska. . . . Yesu anatenga mkate, nadalitsa . . . Ndipo pamene anatenga chikho [vinyo], anayamika . . . “ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.”
Mateyu 26:19–28
Ndipo m’phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera . . . phwando la vinyo wa pamitsokwe . . . Iye wameza imfa kunthawi yonse. . . . Ndipo adzanena tsiku limenelo, “Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa.”
Yesaya 25:6–9
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi