Tsiku la Chitetezero ndi tsiku lalikulu pamene machimo onse a anthu ndi ansembe amakhululukidwa. Aisraeli anayiwala chisomo cha Mulungu ndipo anachimwa polambira fano, mwana wa ng’ombe wa golide. N’chifukwa chake Mose anaphwanya magome amalamulo khumi oyamba operekedwa ndi Mulungu. Aisraele analapa machimo awo ndipo Mulungu anawapatsa gawo lachiwiri la Malamulo Khumi; tsiku limeneli linakhala chiyambi cha Tsiku la Chitetezo.
M’Chipangano Chakale, machimo onse a Aisraele ankasamutsidwa kwa kanthaŵi ku malo opatulikitsa kufikira pa Tsiku la Chitetezero. Lero, machimo athu onse adasamutsidwa kwa Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi, omwe ali zenizeni za malo opatulikitsa. Kenako, pa Tsiku la Chitetezero, machimo athu onse amaperekedwa kwa Satana, yemwe ndi woyambitsa uchimo. Pamapeto pake, Satana adzaweruzidwa kuphompho, ndiko kuti, ku Hade, ndipo pofika nthawi imeneyo, machimo onse adzatha.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Komatu, tsiku lakhumi la mwezi uwu wachisanu ndi chiwiri, ndilo tsiku la chitetezero; mukhale nao msonkhano wopatulikitsa, ndipo mudzichepetse; ndi kubwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova.
Levitiko 23:26-27
M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!
Yohane 1:29
Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya moto ndi sulufure , kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi.
Chivumbulutso 20:10
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi