Mulungu analamula Mose kuti amange chihema kuti aikemo Malamulo Khumi achiwiri. Pamene anthu anazindikira tchimo lawo lomwe lidawachititsa kupwanya Malamulo Khumi oyambirira, iwo analapa ndi kubweretsa mwaufulu zipangizo za chihema. Ichi chinakhala chiyambi cha Phwando la Misasa.
Kenako anamanga misasa m’bwalo la kachisi komanso padenga la kachisi pogwiritsa ntchito nthambi zamitengo yosiyanasiyana.
Phwando la Misasa ndi tsiku limene Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi amasonkhanitsa anthu awo onse pamodzi. Anthu ayenera kuyamika Mulungu amene wawakhululukira ndi kuwapulumutsa ku machimo awo. Ndipo kupyolera mwa Mzimu Woyera wa mvula ya masika imene analandira, iwo ayenera kupeza mamembala onse a m’banja lakumwamba padziko lonse lapansi amene ali zipangizo za Kachisi wakumwamba wa Yerusalemu.
Chifukwa chake Yehova Mulungu wa makamu atero, “…ndidzayesa mau anga akhale m'kamwa mwako ngati moto, anthu awa ndidzayesa nkhuni, ndipo udzawatha iwo.”
Yeremiya 5:14
Mwa Iye chimango chonse cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale Kachisi wopatulika mwa Ambuye; chimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa Mzimu.
Aefeso 2:21-22
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi