Baibulo limachitira umboni kuti angelo akumwamba anaponyedwa padziko lapansili chifukwa chakuti anayesedwa ndi Satana ndi kuchimwa kumwamba—iyi ndi nkhani ya anthu. Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi anabwera ku dziko lino lapansi nakhazikitsa Paska wa pangano latsopano kuti apereke chikhululukiro cha machimo kwa anthu kuti athe kubwerera kumudzi wawo wauzimu, ufumu wamuyaya wakumwamba.
Monga momwe banja lapadziko lapansi limayanjanitsidwa mwa mwazi, banja lakumwamba nalonso limayanjanitsidwanso mwa mwazi. Kuti tikhale mamembala a banja lakumwamba monga ana a Mulungu Atate ndi Mulungu Amayi, anthu ayenera kudya mkate wa Paska ndi kumwa vinyo wa Paska amene ndi thupi ndi mwazi wa Mulungu.
Lero, mamembala a mpingo wa Mulungu m’maiko 175 akusunga Paska ndi maganizo amodzi.
amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema:
Ahebri 8:5
Ndipo tsiku la mikate yopanda chotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paska. . . .
Ndipo m'mene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; . . . Ndipo choteronso chikho, atatha mgonero, nanena, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.
Luka 22:7-20
Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera,
komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;
Aefeso 2:19
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi