Mipingo yonse imavomereza kutchula Mulungu kuti “Atate” mosasamala kanthu za zikhulupiliro zawo.
M’mbiri yonse, anthu adalambira ndi kukhulupirira Mulungu mmodzi yekha, Mulungu Atate, koma Baibulo latiphunzitsa mobwerezabwereza kuti anthu alandire moyo ndi kulowa mu ufumu wamuyaya wakumwamba, kukhalapo kwa Mulungu Amayi ndikofunikira.
Mulungu analenga nsomba za m’nyanja, nyama za m’dziko, mbalame zamlengalenga, dziko la zomera, ngakhalenso anthu kuti alandire moyo kudzera mwa amayi, pofuna kuti tizindikire Mulungu Amayi amene amapereka moyo kudzera mu chisamaliro cha zinthu zonse.
Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu,
kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu;
chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro
chanu zinakhala, ndipo zinalengedwa.
Chivumbulutso 4:11
Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake,
m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye;
adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.
Genesis 1:27
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi