Popeza Mulungu ananena kuti iwo amene amakhulupirira Iye adzalandira Mzimu Woyera, iwo amene akufuna kuulandira ayenera kukhulupirira ndi kutsatira ziphunzitso za Mulungu Yehova mu m'badwo wa Atate, Yesu mu m'badwo wa Mwana, ndi Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amai, amene adza monga Mzimu ndi Mkwatibwi, mu m'badwo wa Mzimu Woyera.
Amene amamvera Mawu a Mulungu ndi amene amakhulupiriradi mwa Mulungu. Monga momwe Nowa, Abrahamu, Mose, Yoswa, ndi Kalebe adadalitsidwira chifukwa chomvera Mawu a Mulungu, momwemonso anthu achikhulupiriro amene amasunga Tsiku la Sabata ndi Paska—Mawu a Mulungu—adzadalitsidwa lero.
“Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu.” Yohane 8:47
Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake. Ndipo anthu onse a pa dziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuopani. Deuteronomo 28:9–10
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi