Monga momwe padziko lapansi
pano pali malamulo, Mulungu alinso
ndi malamulo opulumutsa anthu.
Monga momwe Rehobiamu wa ku Yuda ndi
Yerobiamu wa ku Israyeli anasonyezera
m’mbuyomo, maufumu ndi anthu amene
satsatira malamulo a Mulungu adzalandira
zionongeko ndi chilango pamapeto pake.
Baibulo limanena kuti anthu amene
amasiya chilamulo cha Mulungu
ndi amene amasiya Mulungu.
Pakati pa mipingo yambiri padziko lapansi,
Mulungu ali ndi mpingo umene umasunga
chilamulo cha Mulungu [malamulo] ndi
kuutsogolera ku chimbano pa zionongeko
ngakhalenso pankhondo yaikulu yolimbana ndi Satana.
Ndipo kunachitika, utakhazikika ufumu
wa Rehobowamu, nalimbika iye, anasiya
chilamulo cha Yehova, ndi Aisraele onse pamodzi naye.
Ndipo Rehobowamu atakhala mfumu
zaka zinai, Sisake mfumu ya ku
Ejipito anakwerera Yerusalemu,
popeza iwo adalakwira Yehova.
2 Mbiri 12:1-2
Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, ndipo
chinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala
a mbeu yake, amene asunga malamulo a
Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu. Ndipo
chinjokacho chinakaimirira m’mbali mwa nyanja.
Chivumbulutso 12:17
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi