Monga momwe Mulungu anayesera ndi kuyeretsa mitima ya Aisrayeli m’mnyengo zovuta zosatha pamene anali m’chipululu kwa zaka 40, nthaŵi zambiri timakumana ndi mawu a Mulungu amene ndi ovuta kuwamvera ndi lingaliro lakuti, “Kodi ndingatsatiredi mawu awa?” Komabe, Mulungu amatiyenga ngati golide potilola kumvera mawuwo kuti tithe kubadwanso monga ana a Mulungu ndi kulandira madalitso akumwamba.
Pollyanna wochokera m’buku lotchedwa Pollyanna lofalitsidwa ku America mu 1913 anakondweretsa anthu oyandikana naye kudzera mu masewera ake, “The Glad Game.” Mofanananso, ife, ana a Mulungu, tiyenera kukhala osangalala nthaŵi zonse ndi kuyamika, tikumalingalira za madalitso a Ufumu waulemerero wa Kumwamba umene Mulungu Atate ndi Mulungu Amayi adzatipatsa.
Kondwerani nthawi zonse; Pempherani kosaleka; M’zonse yamikani . . .
1 Atesalonika 5:16–18
Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golide ali ndi ng’anjo; koma Yehova ayesa mitima.
Miyambo 17:3
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi