Phwando la Mkate Wopanda Chotupitsa ndi phwando lakuti tiyang’ane mmbuyo pa moyo ndi masautso a Khristu, kulapa machimo athu, ndi kutaya chikhulupiriro chachibwana. Mofanana ndi mtumwi Paulo, chikhulupiliro chathu chiyenela kukula kusanduka chikhulupililo chokhwima, kuti tiphunzire kukhala oyamika moona pa mavuto ochuluka amene timakumana nawo m’moyo wathu wa chikhulupiliro.
Yesu sanakhale moyo waulemelero ndi ulemu umene zinamuyenerera ngati Mulungu. Anapirira masautso a mtanda chifukwa cha ana Ake pamodzi ndi kunyozedwa ndi kudedwa ndi ena. Chomwemonso, mamembala a Mpingo wa Mulungu amakhala moyo wa ena, osati chimwemwe chawo. Iwo amayesetsa kubadwanso monga anthu amphumphu amene Mulungu amakondwera nawo.
Pomwepo mkulu wa ansembe anang’amba zovala zake, nati, “Achitira Mulungu mwano!
Tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo.Muganiza bwanji?” Iwo anayankha nati, “Ali woyenera kumupha,” Pomwepo iwo anathira malovu pankhope pake, nambwanyula Iye. Ndipo ena anapanda khofu, nati, “Utilote ife, Khristu Iwe.Wakumenya Iwe ndani?”
Mateyu 26:65–68
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi