Mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa
umabweretsa imfa, ndipo mtengo wa
moyo umabweretsa moyo wosatha.
M’munda wa Edeni, Adamu ndi Hava
anathamangitsidwa ndipo anafa chifukwa anadya za
mtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa.
Nkhani imeneyi ikusonyeza kuti anthu
amafa chifukwa chochimwa kumwamba.
Zaka 2,000 zapitazo, Yesu anabwera padziko lapansi pa chipulumutso cha anthu.
Ndipo mu m’badwo wa Mzimu Woyera,
Khristu Ahnsahnghong anabwera ku dziko
lino lapansi ndipo anatipatsa ife moyo wosatha
kupyolera mu Paskha wa pangano latsopano,
umene uli zenizeni za mtengo wa moyo.
Komanso, Khristu Ahnsahnghong, amene anabweretsa
mtengo wa moyo, ndiye Phungu wa Ziyoni
woloseredwa m’buku la Mika.
Iye anatidziwitsa kuti chipulumutso chomaliza
cha anthu chimadalira Mulungu Mayi.
Ndipo anati Yehova Mulungu, Taonani,
munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife,
wakudziwa zabwino ndi zoipa:
ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthawi zonse,
Genesis 3:22
Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo,
Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya
thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi
wake, mulibe moyo mwa inu nokha.
Iye wakudya thupi langa ndi
kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; . . .
Yohane 6:53-54
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi