Mulungu amalamulira dziko lachikhulupiriro, komwe kulibe chomwe sichingatheke ndipo zonse zimakwaniritsidwa monga momwe adakonzera.
Mulungu anagawa Nyanja Yofiira ndi ndodo, nagonjetsa asilikali 135,000 pamodzi ndi asilikali 300 a Gideoni, ndipo anapatsa Aisrayeli chakudya kwa zaka 40 pamene anali m’chipululu. Zonsezi ndi zozizwitsa zomwe Mulungu adachita m'dziko lachikhulupiliro zomwe sizikanatheka mu dziko la ngodya zitatu.
Dziko lakuthupi ndi dziko lachikhulupiriro ndi zosiyana monga mphamvu yokoka yapadziko lapansi ndi ya mwezi. Pamene tizindikira izi ndi kukhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu Amene angathe kuchita chirichonse, ntchito ya chipulumutso cha dziko lonse lapansi, motsogozedwa ndi Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi, idzakwaniritsidwa.
Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.
Mateyu 19:26
“Ndidziwa kuti mukhoza kuchita zonse, ndi kuti palibe choletsa cholingirira chanu chilichonse. Ndani uyu abisa uphungu wosadziwa kanthu? ...”
Yobu 42:2–3
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi